Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 3:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo mfumu idati kwa Hamani, Siliva akhale wako, ndi anthu omwe; ucite nao monga momwe cikukomera.

12. Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lace lakhumi ndi citatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iri yonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa cilembedwe cao, ndi mitundu iri yonse ya anthu monga mwa cinenedwe cao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahaswero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu.

13. Ndipo anatumiza akalata ndi amtokoma ku maiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi citatu la mwezi wakhumi ndi ciwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha.

14. Mau a colembedwaco, ndiwo kuti licitike lamulo m'maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo.

15. Amtokoma anaturuka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'cinyumba ca ku Susani; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mudzi wa Susani unadodoma.

Werengani mutu wathunthu Estere 3