Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 2:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akuru ace onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu.

19. Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yaciwiri Moredekai anali wa m'bwalo la mfumu.

20. Estere sadaulula cibale cace kapena mtundu wace, monga Moredekai adamuuza; popeza Estere anacita mau a Moredekai monga m'mene analeredwa naye.

21. Masiku awa pokhala Moredekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahaswero.

22. Koma cidadziwika ici kwa Moredekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkuru; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Moredekai.

23. Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napacikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anacilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu.

Werengani mutu wathunthu Estere 2