Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Ukuru wa Moredekai

1. Ndipo mfumu Ahaswero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja yamcere.

2. Ndi zocita zonse za mphamvu yace, ndi nyonga zace, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Moredekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizilembedwa kodi m'buku la mbiri ya mafumu a Mediya ndi Perisiya?

3. Pakuti Moredekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahaswero, nakhala wamkuru mwa Ayuda, nabvomerezeka mwa unyinji wa abale ace wakufunira a mtundu wace zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yace yonse.