Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 9:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo lidzakhala pfumbi losalala pa dziko lonse la Aigupto, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zironda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Aigupto.

10. Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zironda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta.

11. Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose cifukwa ca zirondaw; popeza panali zironda pa alembi ndi pa Aaigupto onse.

12. Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvera iwo; moga Yehova adalankhula ndi Mose.

13. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka oulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.

14. Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anayamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi.

15. Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonoogeke pa dziko lapansi.

16. Koma ndithu cifukwa cace ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.

17. Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke?

18. Taona, mawa monga nthawi yino ndidzabvumbitsa mbvumbi wa matalala, sipadakhala unzace m'Aigupto kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.

19. Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.

20. Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ace ndi zoweta zace;

21. koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zace kubusa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 9