Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 9:25-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Aigupto zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.

26. M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israyeli, munalibe matalala.

27. Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndacimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa,

28. Pembani kwa Yehova; cifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.

29. Ndipo Mose ananena naye, Poturuka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.

30. Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu.

31. Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafura, ndi thonje lidayamba maluwa.

32. Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amabzala m'mbuyo.

33. Ndipo Mose anaturuka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ace kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinabvumbanso padziko.

34. Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kucimwa, naumitsa mtima wace, iye ndi anyamata ace.

35. Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalola ana a Israyeli amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 9