Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 9:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2. Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira cigwiritsire,

3. taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa aburu, pa ngamila, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.

4. Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israyeli ndi zoweta za Aigupto; kuti kasafe kanthu kali konse ka ana a Israyeli,

5. Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzacita cinthu ice m'dzikomu.

6. Ndipo m'mawa mwace Yehova anacita cinthuco, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Aigupto; koma sicinafa cimodzi conse ca zoweta za ana a Israyeli.

7. Ndipo Farao anatuma, taonani, sicidafa cingakhale cimodzi comwe ca zoweta za Aisrayeli. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalola anthu amuke.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 9