Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 9:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2. Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira cigwiritsire,

3. taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa aburu, pa ngamila, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.

4. Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israyeli ndi zoweta za Aigupto; kuti kasafe kanthu kali konse ka ana a Israyeli,

5. Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzacita cinthu ice m'dzikomu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 9