27. Timuke ulendo wa masiku atatu m'cipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe.
28. Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova. Mulungu wanu m'cipululu; komatu musamuke kutaritu: mundipembere.
29. Ndipo Mose anati, Onani, ndirikuturuka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza icoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ace, ndi kwa anthu ace; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.
30. Ndipo Mose anaturuka kwa Farao, napemba Yehova.
31. Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nacotsera Farao ndi anyamata ace ndi anthu ace mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.
32. Koma Farao anaumitsa mtima wace nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.