Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 8:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire.

2. Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi acule;

3. ndipo m'nyanjamo mudzacuruka acule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'cipinda cogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'micembo yanu yooceramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo.

4. Ndipo acule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse.

5. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse acule pa dziko la Aigupto.

6. Ndipo Aroni anatambasula dzanja lace pa madzi a m'Aigupto; ndipo anakwera acule, nakuta dziko la Aigupto.

7. Ndipo alembi anacita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa acule pa dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 8