Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:22-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, nchito yoomba ya lamadzi lokha;

23. ndi pakati pace polowa mutu, ngati polowa pa maraya ocingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pace, pangang'ambike.

24. Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25. Ndipo anapanga miriu ya golidi woona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

26. Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.

27. Ndipo anaomba maraya a bafuta, a nchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ace amuna,

28. ndi nduwira va bafuta wa thonje losansitsa, ndi akapal okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zobvala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

29. ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, nchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.

30. Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golidi woona, nalembapo lemba, ngati malocedwe a cosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39