Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:28-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsici ndi masekeli aja cikwi cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yace, nazigwirizitsana pamodzi.

29. Ndi mkuwa wa coperekaco ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.

30. Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi made ace amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,

31. ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku cipata ca pabwalo, ndi ziciri zonse za cihema, ndi ziciri zonse za pabwalo pozungulira.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38