Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wasitimu; utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono itaru.

2. Ndipo anapanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zinakhala zoturuka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.

3. Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zoparira moto; zipangizo zace zonse anazipanga zamkuwa.

4. Ndipo anapangira guwa La nsembelo made, malukidwe ace nja mkuwa, pansi pa matso ace wakulekeza pakati pace.

5. Ndipo anayengera mathungo anai a made amkuwawo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko.

6. Napanga mphiko za mtengo wasitimu, nazikuta ndi mkuwa.

7. Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.

8. Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la cihema cokomanako.

9. Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwela, kumwela, nsaru zocingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;

10. nsici zace makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace zasiliva.

11. Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsici zace makumi awiri, nw makamwa ace makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38