Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 36:25-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndi ku mbali yina ya kacisi, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva;

26. makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

27. Ndi ku mbali ya kumbuyo ya kacisi kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi.

28. Anapanganso matabwa awiri a ku ngondya za kacisi, m'mbali zace ziwirio

29. Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizilca pamodzi pamutu pace ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pa ngondya ziwiri.

30. Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi.

31. Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wasmmu; Isanu ya matabwa a pa mbali yina ya kacisi,

32. ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzace ya kacisi, ndi mitanda lsanu ya matabwa a kacisi ali pa mbali ya kumadzulo.

33. Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo.

34. Ndipo anakuta matabwa ndi golidi, napanga mphete zao zagolidi zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golidi.

35. Ndipo anaomba nsaru yocinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anaciomba ndi akerubi nchito ya mmisiri.

36. Ndipo anaipangira mizati inai yasitimu, nazikuta ndi golidi; zokowera zao zinali zagolidi; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva.

37. Ndipo anaomba nsaru yotsekera pa khomo la cihemaco, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula;

38. ndi nsamamira zace zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golidi; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 36