Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 36:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Anaika magango makumi asanu pa nsaru imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; magango anakomanizana lina ndi linzace.

13. Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolidi, namanga nsaru pamodzi ndi zokowerazo; ndipo kacisi anakhala mmodzi.

14. Ndipo anaomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; anaomba nsaru zophimba khumi ndi imodzi.

15. Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsaru khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao.

16. Ndipo anamanga pamodzi nsaru zisanu pa zokha, ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha.

17. Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo, ya cilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo, ya cilumikizano cina.

18. Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.

19. Ndipo anasokera hemalo cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi cophimba ca zikopa za akatumbu pamwamba pace.

20. Ndipo anapanga matabwa a kacisi, oimirika, a mtengo wasitimu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 36