Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 34:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi, nalambira.

9. Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopane pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi ucimo wathu, ndipo mutilandire tikhale colowa canu.

10. Ndipo iye anati, Taona, Ine ndicita pangano; ndidzacita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinacitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uti wonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona nchito ya Yehova, pakuti cinthu ndikucitiraci ncoopsa.

11. Dzisungire cimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

12. Dzicenjere ungacite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;

13. koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

14. pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lace ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

15. ungacite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angacite cigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zace;

16. ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangacite cigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kucititsa ana anu amuna cigololo potsata milungu yao.

17. Usadzipangire milungu yoyenga.

18. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa. Uzidya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unaturuka m'Aigupto.

19. Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.

20. Koma woyamba wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 34