Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 34:10-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo iye anati, Taona, Ine ndicita pangano; ndidzacita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinacitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uti wonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona nchito ya Yehova, pakuti cinthu ndikucitiraci ncoopsa.

11. Dzisungire cimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

12. Dzicenjere ungacite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;

13. koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;

14. pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lace ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

15. ungacite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angacite cigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zace;

16. ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangacite cigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kucititsa ana anu amuna cigololo potsata milungu yao.

17. Usadzipangire milungu yoyenga.

18. Uzisunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa. Uzidya mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unaturuka m'Aigupto.

19. Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa.

20. Koma woyamba wa buru uzimuombola ndi mwana wa nkhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.

21. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira nchito, koma lacisanu ndi ciwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula.

22. Ndipo uzicita madyerero a masabata, ndiwo madyerero a zipatso zoyamba za masika a tirigu, ndi madyerero a kututa pakutha pa caka.

23. Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, katatu caka cimodzi.

24. Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu caka cimodzi.

25. Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m'mawa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 34