Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 31:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

13. Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.

14. Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; ali yense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti ali yense wakugwira nchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wace.

15. Agwire nchito masiku asanu ndi limodzi; koma lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; ali yense wogwira nchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.

16. Cifukwa cace ana a Israyeli azisunga Sabata, kucita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha;

17. ndico cizindikilo cosatha pakati pa Ine ndi ana a Israyeli; pakuti Yehova analenga zam'mwamba ndi dziko lapansi masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lacisanu ndi ciwiri, naonanso mphamvu.

18. Ndipo atatha iye kulankhula ndi Mose, pa phiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi cala ca Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 31