Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:7-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Aroni azifukizapo cofukiza ca zonunkhira zokoma m'mawandim'mawa, pamene akonza nyalizo, acifukize.

8. Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, acifukize cofukiza cosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu,

9. Musafukizapo cofukiza cacilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena copereka; musathirepo nsembe yothira.

10. Ndipo Aroni azicita coteteza pa nyanga zace kamodzi m'caka; alicitire coteteza ndi mwazi wa nsembe yaucimo ya coteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulikitsa la Yehova.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12. Pamene uwerenga ana a Israyeli, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova ciombolo ca pa moyo wace, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.

13. Ici acipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo copereka ca Yehova.

14. Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zace, apereke coperekaco kwa Yehova.

15. Wacuma asacurukitsepo, ndi osauka asacepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka copereka kwa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.

16. Ndipo uzilandira ndarama za coteteza kwa ana a Israyeli, ndi kuzipereka pa nchito ya cihema cokomanako; kuti zikhale cikumbutso ca ana a Israyeli pamaso pa Yehova, kucita coteteza ca miyoyo yanu.

17. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,

18. Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lace lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa ciliema cokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

19. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;

20. pakulowa iwo m'cihema cokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

21. asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zace, mwa mibadwo yao.

22. Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30