Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 30:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wasitimu.

2. Utali wace ukhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono; likhale lampwamphwa; ndi msinkhu wace mikono iwiri; nyanga zace zituruke m'mwemo.

3. Ndipo ulikute ndi golidi woona, pamwamba pace ndi mbali zace zozungulira, ndi nyanga zace; ulipangirenso mkombero wagolidi pozungulira,

4. Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolidi pansi pa mkombero wace; uziike pa nthiti zace ziwiri, pa mbali zace ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

5. Ndipo upange mphiko za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi.

6. Nuliike cakuno ca nsaru yocinga iri ku likasa la mboni, patsogolo pa cotetezerapo ciri pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.

7. Ndipo Aroni azifukizapo cofukiza ca zonunkhira zokoma m'mawandim'mawa, pamene akonza nyalizo, acifukize.

8. Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, acifukize cofukiza cosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu,

9. Musafukizapo cofukiza cacilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena copereka; musathirepo nsembe yothira.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 30