Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.

7. Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza.

8. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati.

9. Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m'cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ace amuna,

10. Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.

11. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.

12. Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi cala cako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.

13. Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi cokuta ca mphafa ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe.

14. Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi cikopa cace, ndi cipwidza cace, uzitentha izi ndi moto kunja kwa cigono; ndiyo nsembe yaucimo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29