Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako indi kuwasambitsa m'madzi.

5. Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m'cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;

6. ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.

7. Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza.

8. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati.

9. Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m'cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ace amuna,

10. Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.

11. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29