Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:23-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosanganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, ziri mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;

24. ndipo uike zonsezo m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ace amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

25. Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zicite pfungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

26. Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

27. Ndipo upatule nganga va nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ace amuna;

28. ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ace amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israyeli; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israyeli, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

29. Ndipo zobvala zopatulika za Aroni zikhale za ana ace amuna pambuyo pace, kuti awadzoze atazibvala, nadzaze manja ao atazibvala;

30. mwana wace wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwace azibvala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'cihema cokomanako kutumikira m'malo opatulika.

31. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nayama yace m'malo opatulika.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29