Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ici ndico uwacitire kuwapatula, andicitire nchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,

2. ndi mkate wopanda cotupitsa, ndi timitanda topanda cotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda cotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu.

3. Ndipo uziike mu mtanga umodzi, ndi kubwera nazo mumtanga, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.

4. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako indi kuwasambitsa m'madzi.

5. Pamenepo utenge zobvalazo ndi kubveka Aroni maraya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi capacifuwa, ndi kummangira m'cuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru;

6. ndipo uike nduwira pamutu pace, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo.

7. Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pace, ndi kumdzoza.

8. Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati.

9. Uwamangirenso Aroni ndi ana ace amuna mipango m'cuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ace amuna,

10. Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo Aroni ndi ana ace amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.

11. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la cihema cokomanako.

12. Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi cala cako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe.

13. Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi cokuta ca mphafa ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29