Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 27:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo pa cipata ca bwalolo pakhale nsaru yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula; nsici zace zikhale zinai, ndi makamwa ao anai.

17. Nsici zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.

18. Utali wace wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwace makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wace wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsicizo akhale amkuwa.

19. Zipangizo zonse za kacisi, m'macitidwe ace onse, ndi ziciri zace zonse, ndi ziciri zonse za bwalo lace, zikhale zamkuwa.

20. Ndipo uuze ana a Israyeli akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.

21. Aroni ndi ana ace aikonze m'cihema cokomanako, kunja kwa nsaru yocinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 27