Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 27:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wasitimu, utali wace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, guwa la nsembelo likhale lampwamphwa, ndi msinkhu wace mikono itatu.

2. Ndipo uzipanga nyanga zace pa ngondya zace zinai; nyanga zace zikhale zoturuka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa:

3. Ndipo uzipanga zotayira zace zakulandira mapulusa ace, ndi zoolera zace, ndi mbale zowazira zace, ndi mitungo yace, ndi zoparira moto zace; zipangizo zace zonse uzipanga zamkuwa.

4. Ndipo ulipangire made, malukidwe ace ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngondya zace zinai mphete zinai zamkuwa.

5. Nuwaike pansi pa matso a guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 27