Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 26:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolidi, ndi kumanga nsaruzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti kacisi akhale mmodzi.

7. Ndipo uziomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; uziomba nsaru khumi ndi imodzi.

8. Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsarukhumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.

9. Nuzisoka pamodzi nsaru zisanu pa zokha ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsaru yacisanu ndi cimodziyo pa khomo la hema.

10. Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo ya cilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo ya cilumikizano cina.

11. Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.

12. Ndipo cotsalaco pa nsaru za hemalo, hafu yace ya nsaru yotsalirayo, icinge pambuyo pace pa kacisi.

13. Ndi mkono wa pa mbali yino, ndi mkono wa pa mbali inzace, wakutsalira m'utali wace wa nsaru za hemalo, icinge pambali zace za kacisi, mbali yino ndi mbali yina, kumphimba.

14. Ndipo uzipangira hema cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi cophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 26