Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 26:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo uzipangira kacisi matabwa oimirika, a mtengo wasitimu.

16. Utali wace wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwace kwa thabwali mkono ndi hafu.

17. Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a kacisi.

18. Ndipo uzipanga matabwa a kacisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwela, kumwela.

19. Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri;

20. ndi pa mbali yace yina ya kacisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai;

21. makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.

22. Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya kacisi ya kumbuyo kumadzulo.

23. Nupange matabwa awiri a ngondya za kacisi za kumbuyo.

24. Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwace ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala a ngondya ziwiri.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 26