Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 25:31-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo uzipanga coikapo nyali ca golidi woona; coikapoco cisulidwe mapangidwe ace, tsinde lace ow thupi lace; zikho zace, mitu yace, ndi maluwa ace zikhale zocokera m'mwemo;

32. ndipo m'mbali zace muturuke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali yace yina, ndi mphanda zitatu za coikapo nyalico zituruke m'mbali inzace.

33. Ku mphanda yina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzace zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

34. Ndipo pa coikapo nyali comwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yace ndi maluwa ace;

35. pakhale mutu pansi pa mphaada ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zoturuka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zoturuka m'coikapo nyalico.

36. Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zoturuka m'mwemo; conseci cikhale cosulika cimodzi ca golidi woona.

37. Ndipo uzipanga nyali zace, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zace, ziwale pandunji pace.

38. Ndipo mbano zace, ndi zoolera zace, zikhale za golidi woona.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 25