Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 23:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Uzibweca nazo zoyambayamba za m'munda mwako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.Mulungu aloniezana nao za Kanani.

20. Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamalo pomwe ndakonzeratu.

21. Musamalire iye, ndi kumvera mau ace; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zoo lakwa zanu; popeza dzina langa liri m'mtima mwace.

22. Pakuti ukamveratu mau ace, ndi kucita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.

23. Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga.

24. Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kucita monga mwa nchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 23