Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 22:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Munthu akaikiza ndalama kapena cuma kwa mnansi wace, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe cowirikiza.

8. Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lace pa cuma ca mnansi wace.

9. Mlandu uti wonse wa colakwa, kunena za ng'ombe, za buru, za nkhosa, za cobvala, za kanthu kali konse kotayika, munthu anenako kali kace; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe cowirikiza kwa mnansi wace.

10. Munthu akaikiza buru, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena coweta cina kwa mnansi wace, ndipo cikafa, kapena ciphwetekwa, kapena wina acipitikitsa osaciona munthu;

11. lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanaturutsa dzanja lace pa cuma ca mnansi wace; ndipo mwiniyo azibvomereza, ndipo asalipe.

12. Koma ngati cidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo.

13. Ngati cajiwa ndithu, abwere naco cikhale mboni; asalipe pa cojiwaco.

14. Munthu akabwereka cinthu kwa mnansi wace, ndipo ciphwetekwa, kapena cifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 22