Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 21:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wace.

22. Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.

23. Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo,

24. diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,

25. kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.

26. Munthu akampanda mnyamata wace, kapena mdzakazi wace, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu cifukwa ca diso lace.

27. Ndipo akagurula dzino la mnyamata wace, kapena dzino la mdzakazi wace, azimlola amuke waufulu cifukwa ca dzino lace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 21