Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 21:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Munthu wakutemberera atate wace, kapena amai wace, aphedwe ndithu.

18. Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzace ndi mwala, kapena ndi nkhonyo, wosafa iye, koma wakhulungira pakama;

19. akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yace, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pace pokha azimbwezera, namcizitse konse.

20. Munthu akakantha mnyamata wace, kapena mdzakazi wace, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pace; ameneyo aliridwe ndithu.

21. Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wace.

22. Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 21