3. Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.
4. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;
5. usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
6. ndi kuwacitira cifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.
7. Usaehule dzina la Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa, amene achula pacabe dzina lacelo.
8. Uzikumbukila tsiku la Sabata, likhale lopatulika.
9. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumariza nchito zako zonse;