Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 20:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Usacite cigololo.

15. Usabe.

16. Usamnamizire mnzako.

17. Usasirire nyumba yace ya mnzako, usasirire mkazi wace wa mnzako, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, kapena ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.

18. Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga, ndi phiri lirikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.

19. Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe,

20. Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa iye kukhale pamaso panu, kuti musacimwe.

21. Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukuru kuli Mulungu.

22. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israyeli, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kucokerakumwamba.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 20