Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 2:21-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo Mose anabvomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wace wamkazi Zipora.

22. Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamucha dzina lace Gerisomu; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.

23. Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aigupto; ndi ana a Israyeli anatsitsa moyo cifukwa ca ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungucifukwa ca ukapolowo.

24. Ndipo Molungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukila cipangano cace ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo.

25. Ndipo Molungu anapenya Aisrayeli, ndi Mulungu anadziwa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 2