Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 2:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. M'mawa mwace anaturukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wocimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?

14. Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkuru ndi woweruza wathu? kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha M-aigupto? Ndipo Mose anacita mantha, nanena, Ndithu cinthuci cadziwika.

15. Pamene Farao anacimva ici, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midyani; nakhala pansi pacitsime.

16. Ndipo wansembe wa Midyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimweco kuti amwetse gulu la atate wao.

17. Pamenepo anadza abusa nawapitikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

18. M'mene anafika kwa Rehueli atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

19. Ndipo anati two, Munthu M-aigupto anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

20. Ndipo anati kwa ana ace akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye cakudya.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 2