Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anacoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israyeli linalowa m'cipululu ca Sini, ndico pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi waciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto.

2. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linadandaulira Mose ndi Aroni m'cipululu;

3. nanena nao ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife cokhuta; pakuti mwatiturutsa kudza nafe m'cipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.

4. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzabvumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituruka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lace, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'cilamulo canga kapena iai.

5. Ndipo kudzakhala tsiku lacisanu ndi cimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataoniezapo muyeso unzace wa pa tsiku limodzi.

6. Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israyeli, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakuturutsani m'dziko la Aigupto;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16