Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, cifukwa cace tsiku lacisanu ndi cimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwace, munthu asaturuke m'malo mwace tsiku lacisanu ndi ciwiri.