Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:25-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.

26. Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.

27. Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anaturuka kukaola, koma sanaupeza.

28. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira titi?

29. Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, cifukwa cace tsiku lacisanu ndi cimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwace, munthu asaturuke m'malo mwace tsiku lacisanu ndi ciwiri.

30. Ndipo anthu anapumula tsiku lacisanu ndi ciwiri.

31. Ndipo mbumba ya Israyeli inaucha dzina lace Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosanganiza ndi uci.

32. Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'cipululu, muja ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto.

33. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16