Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.

20. Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

21. Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.

22. Ndipo kunali tsiku lacisanu ndi cimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzace, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.

23. Ndipo ananena nao, Ici ndi comwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; cimene muzioca, ocani, ndi cimene muziphika phikani; ndi cotsala cikukhalireni cosunguka kufikira m'mawa.

24. Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi.

25. Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.

26. Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.

27. Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anaturuka kukaola, koma sanaupeza.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16