Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 16:12-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndamva madandaulo a ana a Israyeli; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

13. Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.

14. Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa cipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati cipale panthaka.

15. Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,

16. Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yace; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwace.

17. Ndipo ana a Israyeli anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono.

18. Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yace.

19. Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa.

20. Koma sanammvera Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao.

21. Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yace; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.

22. Ndipo kunali tsiku lacisanu ndi cimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzace, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose.

23. Ndipo ananena nao, Ici ndi comwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; cimene muzioca, ocani, ndi cimene muziphika phikani; ndi cotsala cikukhalireni cosunguka kufikira m'mawa.

24. Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi.

25. Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo.

26. Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 16