Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 15:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga,Ndipo wakhala cipulumutso canga;Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza:Ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzammveketsa.

3. Yehova ndiye wankhondo;Dzina lace ndiye Yehova.

4. Magareta a Farao ndi nkhondo yace anawaponya m'nyanja;Ndi akazembe ace osankhika anamira m'Nyanja Yofiira.

5. Nyanja inawamiza:Anamira mozama ngati mwala.

6. Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.

7. Ndipo ndi ukulu wanu waukuru mwapasula akuukira Inu;Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati ciputu.

8. Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.

9. Mdani anati,Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha;Ndidzakhuta nao mtima;Ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.

10. Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;Anamira m'madzi akuru ngati mtobvu.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 15