Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 12:39-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo anaoca timitanda topanda cotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Aigupto, popeza sadaikamo cotupitsa; pakuti adawapitikitsa ku Aigupto, ndipo sanathe kucedwa, kapena kudzikonzeratu kamba.

40. Ndipo kukhala kwa ana a Israyeli anakhala m'Aigupto ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu.

41. Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anaturuka m'dziko la Aigupto.

42. Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, cifukwa ca kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israyeli ku mibadwo yao.

43. Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paskha ndi ili: mwana wa mlendo ali yense asadyeko;

44. koma kapolo wa mwini ali yense, wogula ndi ndarama, utamdula, ndipo adyeko.

45. Mlendo kapena wolembedwa nchito asadyeko.

46. Audye m'nyumba imodzi; usaturukira nayo kubwalo nyama yina; ndipo musathyole pfupa lace.

47. Msonkhano wonse wa Israyeli uzicita ici.

48. Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paskha, adulidwe amuna ace onse, ndipo pamenepo asendere kuucita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa ali yense asadyeko.

49. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.

50. Ndipo ana onse a Israyeli anacita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anacita.

51. Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anaturutsa ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, monga mwa makamu ao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 12