Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 10:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wace, ndi mtima wa anyamata ace, kuti ndiike zizindikilo zanga izi pakati pao;

2. ndi kuti ufotokozere, m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, comwe ndidzacita m'Aigupto, ndi zizindikilo zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.

3. Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzicepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;

Werengani mutu wathunthu Eksodo 10