Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 8:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.

5. Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.

6. Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.

7. Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe, ndi la maiwe akuturuka m'zigwa, ndi m'mapiri;

8. dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uci;

9. dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yace nja citsulo, ndi m'mapiri ace mukumbe mkuwa.

10. Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu cifukwa ca dziko lokomali anakupatsani.

11. Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;

12. kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13. ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;

14. mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo;

15. amene anakutsogolerani m'cipululu cacikuru ndi coopsaco, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakuturutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;

16. amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 8