Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 6:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo mau awa ndikuuzanilero, azikhala pamtima panu;

7. ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

8. Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati cizindikilo, ndipo akhale ngati capamphumi pakati pa maso anu.

9. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.

10. Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;

11. ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;

12. pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,

13. Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 6