Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:28-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, nchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza.

29. Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

30. Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ace;

31. popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wacifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala cipangano ca makolo anu cimene analumbirira iwo.

32. Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzace a thambo, ngati cinthu cacikuru conga ici cinamveka, kapena kucitika?

33. Kodi pali mtundu wa anthu udamva a Malungu akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo?

34. Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikilo, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikuru, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakucitirani m'Aigupto pamaso panu?

35. Inu munaciona ici, kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda iye.

36. Anakumvetsani mau ace kucokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wace waukuru; nimunamva mau ace pakati pa moto.

37. Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakuturutsani pamaso pace ndi mphamvu yace yaikuru, m'Aigupto;

38. kupitikitsa amitundu akuru ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale colowa canu, monga lero lino.

39. Potero dziwani lero tino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi pa dziko lapansi; palibe wina.

40. Muzisunga malemba ace, ndi malamulo ace, amene ndikuzuzani lero lino, kuti cikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu acuruke pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.

41. Pamenepo Mose anapatula midzi itatu tsidya lija la Yordano loturuka dzuwa;

42. kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wace dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo:

43. ndiyo Bezere, m'cipululu, m'dziko lacidikha, ndiwo wa Anrubeni; ndi Ramoti m'Gileadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basana, ndiwo wa Amanase.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4