Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawacite m'dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanu lanu.

15. Potero dzicenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenya mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu m'Horebe, ali pakati pa moto;

16. kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga cifaniziro ciri conse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi;

17. mafanidwe a nyama iri yonse iri pa dziko lapansi, mafanidwe a mbalame iri yonse yamapiko yakuuluka m'mlengalenga,

18. mafanidwe a cinthu ciri conse cokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iri yonse yokhala m'madzi pansi pa dziko;

19. ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse.

20. Koma Yehova anakutengani, nakuturutsani m'ng'anjo yamoto, m'Aigupto, mukhale kwa iye anthu a colowa cace, monga mukhala lero lino.

21. Yehova anakwiyanso nane cifukwa ca mau anu, nalumbira kuti sindidzaoloka Yordano ine, ndi kuti sindidzalowa m'dziko lokomali Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu;

22. pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordano; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanu lanu.

23. Dzicenjerani, mungaiwale cipangano ca Yehova Mulungu wanu, cimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, cifaniziro ca kanthu kali konse Yehova Mulungu wanu anakuletsani.

24. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4