Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 34:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.

5. Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Moabu, monga mwa mau a Yehova.

6. Ndipo iye anamuika m'cigwa m'dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwace kufikira lero lino.

7. Ndipo zaka zace za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lace silinacita mdima, ndi mphamvu yace siidaleka.

8. Ndipo ana a Israyeli analira Mose m'zidikha za Moabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose.

9. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ace; ndi ana a Israyeli anamvera iye, nacita monga Yehova adauza Mose.

10. Ndipo sanaukanso mnereri m'lsrayeli ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 34