Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 33:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anati,Yehova anafuma ku Sinai,Nawaturukiraku Seiri;Anaoneka wowala pa phiri la Parana,Anafumira kwa opatulika zikwi zikwi;Ku dzanja lamanja lace kudawakhalira lamulo lamoto.

3. Inde akonda mitundu ya anthu;Opatulidwa ace onse ali m'dzanjamwanu;Ndipo akhala pansi ku mapazi anu;Yense adzalandirako mau anu.

4. Mose anatiuza cilamulo,Colowa ca msonkhano wa Yakobo.

5. Ndipo iye anali mfumu m'Yesuruni,Pakusonkhana mafumu a anthu,Pamodzi ndi mapfuko a Israyeli.

6. Rubeni akhale ndi moyo, asafe,Koma amuna ace akhale owerengeka.

7. Za Yuda ndi izi; ndipo anati,Imvani, Yehova, mau a Yuda,Ndipo mumfikitse kwa anthu ace;Manja ace amfikire;Ndipo mukhale inu thandizo lace pa iwo akumuukira.

8. Ndipo za Levi anati,Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu,Amene mudamuyesa m'Masa,Amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba;

9. Amene anati za atate wace ndi amai wace, Sindinamuone;Sanazindikira abale ace,Sanadziwa ana ace omwe;Popeza anasamalira mau anu, Nasunga cipangano canu.

10. Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu,Ndi Israyeli cilamulo canu;Adzaika cofukiza pamaso panu,Ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu.

11. Dalitsani, Yehova, mphamvu yace,Nimulandire nchito ya manja ace;Akantheni m'cuuno iwo akumuukira,Ndi iwo akumuda, kuti asaukenso.

12. Za Benjamini anati,Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi iye mokhazikika;Amphimba tsiku lonse,Inde akhalitsa pakati pa mapewa ace.

13. Ndipo za Yosefe anati,Yehova adalitse dziko lace;Ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame,Ndi madzi okhala pansipo;

14. Ndi zipatso zofunikatu za dzuwa,Ndi zomera zofunikatu za mwezi,

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 33